CDEDI PRESS BRIEFING - NAMIWA WATOKOTA ZA MAVUTO A FUEL| ATOLANKHANI AMPANIKIZA NDI MAFUNSO AWA
Автор: AM TV MALAWI
Загружено: 2026-01-20
Просмотров: 2047
Bungwe la Center for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) lapempha boma kuti lichite mgwilizano ndi maiko komanso makampani omwe amagulitsa mafuta agalimoto zomwe zithandizile dziko lino kukhala ndi mafuta agalimoto otsika mtengo.
Mkulu wabungweli a Sylvester Namiwa ayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani omwe bungweli likuchititsa ku munzinda wa Lilongwe.
Malingana ndi a Namiwa, dziko lino likukumana ndimavuto okhudza mafuta agalimoto kaamba koti chipani chakale cholamula cha Malawi Congress (MCP) chinasokoneza ndondomeko zoyenela zakagulidwe kamafuta.
Apa Iwo ati bungwe lawo lichita kafukufuku ndikubweletsa poyela zifukwa zomwe boma lakwezela mitengo ya mafuta agalimoto ndikupitilita kupempha boma kutsitsa mtengo wamafutawa.
Pakadalipano, a Namiwa ati akuyembekezela kuti boma lichitapo kanthu potsitsa mtengo wa mafutawa potengela kuti mtsogoleri wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika amamva madandaulo a anthu.
Доступные форматы для скачивания:
Скачать видео mp4
-
Информация по загрузке: